Joshua 11:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Yoswa adagonjetsa dziko lonselo potsata mau amene Chauta adaalamula Mose. Chauta adapereka dziko kwa Aisraele kuti likhale lao, ndipo adaligaŵagaŵa kuti fuko lililonse likhale ndi gawo lake. Motero anthu onse adapumula osamenyanso nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israele, likhale laolao, fuko lililonse gawo lake. Ndipo dziko linapumula nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yoswa anagonjetsa dziko lonse monga momwe Yehova analamulira Mose. Tsono Yoswa analipereka kwa Aisraeli kuti likhale lawo, fuko lililonse gawo lake. Anthu onse anapumula, osamenyanso nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israyeli, likhale lao lao, pfuko liri lonse gawo lace. Ndipo dziko linapumula nkhondo.