Joshua 11:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafumuwo adabwera ndi ankhondo ao onse, ndipo kuchuluka kwao kwa ankhondowo kunali ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Anali ndi akavalo ambiri, pamodzi ndi magaleta omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuluka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kuchuluka kwao ngati mchenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magaleta ambirimbiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafumuwo anabwera pamodzi ndi ankhondo awo onse. Gulu la ankhondo linali lalikulu ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Analinso ndi akavalo ndi magaleta ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturuka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kucuruka kwao ngati mcenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magareta ambirimbiri.