Joshua 11:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauza Yoswa kuti, “Usaŵaope amenewo. Maŵa pa nthaŵi yonga yomwe ino, adzaphedwa onsewo. Akavalo ao muŵalumaze, ndipo mutenthe magaleta ao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; uziwadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope chifukwa mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzawapereka kuti muwaphe. Akavalo awo muwadule matsinde ndipo magaleta awo muwatenthe ndi moto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope cifukwa ca iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israyeli; uziwadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agareta ao ndi moto.