Joshua 11:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yoswa adangoŵachita zomwe Chauta adalamula. Adalumaza akavalo, natentha magaleta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anawachitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magaleta ao ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswa anawachita zimene Yehova analamula. Iye anadula matsinde a akavalo awo ndi kutentha magaleta awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anawacitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magareta ao ndi moto.