Joshua 12:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele anali atagonjetsa dziko lonse la kuvuma kwa Yordani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni m'chigwa cha Yordani, mpaka kumpoto ku phiri la Heremoni ndi dera lonse la kuvuma kwa Araba, ndipo adakhazikika pa dziko lonselo. Mafumu amene adaŵagonjetsawo ndi aŵa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israele anawakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordani kum'mawa, kuyambira chigwa cha Arinoni, mpaka phiri la Heremoni, ndi chidikha chonse cha kum'mawa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israyeli anwakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordano kum'mawa, kuyambira cigwa ca Arimoni, mpaka phiri la Herimoni, ndi cidikha conse ca kum'mawa;