Joshua 12:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sihoni mfumu ya Aamori amene ankakhala ku Hesiboni. Iyeyu ankalamulira kuyambira ku Aroere, mzinda umene uli pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki ku malire a dziko la Aamoni, ndiponso kuphatikizapo theka la dera la Giliyadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sihoni mfumu ya Aamori wokhala m'Hesiboni, wochita ufumu kuyambira ku Aroere ndiwo m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi pakati pa chigwa ndi pa Giliyadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sihoni mfumu ya Aaroori wokhala m'Hesiboni, wocita ufumu kuyambira ku Aroeri ndiwo m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi pakati pa cigwa ndi pa Gileadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;