Joshua 12:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ufumu wake unkafika mpaka ku phiri la Heremoni ndi ku Saleka, ndi ku Basani yense, mpaka ku malire a Agesuri ndi a Amakati. Ufumuwo unkaphatikizanso theka la Giliyadi, kufikira ku dziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nachita ufumu m'phiri la Heremoni, ndi m'Saleka, ndi m'Basani lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Giliyadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nacita ufumu m'phiri la Herimoni, ndi m'Saleka, ndi m'Basana lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Gileadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni.