Joshua 12:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose pamodzi ndi Aisraele adaaŵagonjetsa onsewo, ndipo Mose mtumiki wa Chauta adaapereka maiko aoŵa kwa fuko la Rubeni ndi la Gadi, ndiponso kwa theka la fuko la Manase, kuti akhale choloŵa chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israele anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi fuko la Manase logawika pakati, likhale cholowa chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israyeli anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi pfuko la Manase logawika pakati, likhale colowacao.