Joshua 12:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yoswa ndi Aisraele anali atagonjetsa mafumu onse okhala m'dziko la kuzambwe kwa Yordani, kuyambira ku Bala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni, mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa adagaŵira mafuko a Aisraele dziko limenelo, kuti likhale choloŵa chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israele anawakantha tsidya lija la Yordani kumadzulo, kuyambira Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni mpaka phiri la Halaki lokwera kunka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mafuko a Israele, likhale laolao, monga mwa magawo ao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israyeli anawakantha tsidya lija la Yordano kumadzulo, kuyambira Baala-gadi m'cigwa ca Lebano mpaka phiri la Halaki lokwera kumka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mapfuko a Israyeli, likhale lao lao, monga mwa magawo ao;