Joshua 13:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Yoswa anali atakalamba kwambiri. Tsono Chauta adamuuza kuti, “Tsopanotu iwe wakalamba kwambiri, koma dziko losalandidwa likalipo lalikulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikulukulu, alilandire cholowa chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswa atakalamba Yehova anamuwuza kuti, Iwe tsopano wakalamba kwambiri, koma dziko losalandidwa lilipobe lalikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikurukuru, alilandire colowa cao,