Joshua 13:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ku Basani lidaphatikizapo dziko la Ogi amene ankalamula ku Asitaroti ndi ku Ederei. (Ogi anali yekhayo mfumu ya Arefaimu amene adatsalako). Mose anali atagonjetseratu anthu ameneŵa ndi kuŵapirikitsira kutali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ufumu wonse wa Ogi m'Basani, wa kuchita ufumu m'Asitaroti, ndi m'Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Linaphatikizanso dziko la mfumu Ogi ya ku Basani imene imalamulira kuchokera ku Asiteroti ndi Ederi. Iye yekha ndiye anali mfumu ya Arefaimu amene anapulumuka. Mose anali atawagonjetsa anthu amenewa ndi kuwathamangitsira kutali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ufumu wonse wa Ogi m'Basana, wakucita ufumu m'Asitarotu, ndi m'Edrei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefai); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.