Joshua 13:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe Mose sadapereke dziko kwa fuko la Levi. Zimene ankalandira iwowo ngati choloŵa chao ndi gawo la zopereka zopsereza zimene anthu ankapereka kwa Chauta, monga momwe Chauta adaauzira Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma fuko la Levi sanalipatse cholowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israele, zochitika ndi moto, ndizo cholowa chake, monga Iye adanena naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mose sanapereke dziko kwa fuko la Alevi popeza zopereka zopatulika zimene anthu ankapereka kwa Yehova, Mulungu wa Israeli, ndizo zinali cholowa chawo monga Yehova anawalonjezera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pfuko la Levi sanalipatsa colowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israyeli, zocitika ndi moto, ndizo colowa cace, monga iye adanena naye.