Joshua 13:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imeneyi ndiyo mizinda yonse yakuchigwa, mizinda yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni. Mose anali atagonjetsa Sihoni pamodzi ndi onse olamulira ku Midiyani monga: Evi, Rekemu, Zeri, Huri ndi Reba. Onseŵa ankalamulira dzikolo ngati anyakwaŵa a Sihoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi midzi yonse ya kuchidikha, ndi ufumu wonse wa Sihoni mfumu ya Aamori, wochita ufumu m'Hesiboni, amene Mose anamkantha pamodzi ndi akalonga a Midiyani, Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri ndi Reba, akalonga a Sihoni, nzika za m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzikolo linaphatikizanso mizinda yonse ya ku madera okwera ndiponso dziko lonse la mfumu Sihoni ya Aamori amene ankalamulira kuchokera ku Hesiboni. Mose anamugonjetsa iye pamodzi ndi mafumu a Amidiyani awa: Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu amene anagwirizana ndi Sihoni. Onsewa analamulira dzikolo ngati nduna za Sihoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi midzi yonse ya kucidikha, ndi ufumu wonse wa Sihoni mfumu ya Aamori, wocita ufumu m'Hesiboni, amene Mose anamkantha pamodzi ndi akalonga a Midyani, Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri ndi Reba, akalonga a Sihoni, nzika za m'dziko.