Joshua 13:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtsinje wa Yordani ndiwo unali malire a fuko la Rubeni. Mizinda imeneyo pamodzi ndi midzi yake ndi imene idapatsidwa kwa mabanja a fuko la Rubeni, kuti ikhale choloŵa chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo malire a ana a Rubeni ndiwo Yordani ndi malire ake. Ndicho cholandira cha ana a Rubeni monga mwa mabanja ao, midzi yake ndi milaga yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malire a fuko la Rubeni anali mtsinje wa Yorodani. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake zinapatsidwa kwa mabanja a fuko la Rubeni kuti akhale cholowa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo malire a ana a Rubeni ndiwo Yordano ndi malire ace. Ndico colandira ca ana a Rubeni monga mwa mabanja ao, midzi yace ndi miraga yace.