Joshua 13:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'chigwa cha Yordani adalandiramo Beteharamu, Betenimura, Sukoti ndi Safoni, kudzanso theka la dziko la Sihoni, mfumu ya ku Hesiboni. Malire ake akuzambwe anali mtsinje wa Yordani kufikira ku nyanja ya Galilea chakumpoto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo m'chigwa Beteharamu, ndi Betenimura, ndi Sukoti, ndi Zafoni, chotsala cha ufumu wa Sihoni mfumu ya Hesiboni, Yordani ndi malire ake, mpaka malekezero a nyanja ya Kinereti, tsidya lija la Yordani kum'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mu chigwa cha Yorodani analandiramo Beti-Haramu, Beti-Nimira, Sukoti ndi Zafoni pamodzi ndi dziko lonse la mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. Malire ake a ku madzulo anali mtsinje wa Yorodani kufikira ku Nyanja ya Kinereti, kumpoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo m'cigwa Betiharamu, ndi Beti-nimra, ndi Sukoti, ndi Zafoni, cotsala ca ufumu wa Sihoni mfumu ya Hesiboni, Yoidano ndi malire ace, mpaka malekezero a nyanja ya Kinereti, tsidya lija la Yordano kum'mawa.