Joshua 13:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose anali atapereka kale gawo lina la dziko kwa mabanja a theka la fuko la Manase lija, kuti likhale choloŵa chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mose anaperekanso cholowa kwa fuko la Manase logawika pakati, ndicho cha fuko la Manase logawika pakati monga mwa mabanja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anali atapereka kale gawo lina la dziko limeneli kwa theka la mabanja a fuko la Manase kuti likhale cholowa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mose anaperekanso colowa kwa pfuko la Manase logawika pakati, ndico ca pfuko la Manase logawika pakati monga mwa mabanja ao.