Joshua 13:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
(dziko limene layambira ku mtsinje wa Sihori kuvuma kwa Ejipito mpaka ku malire a Ekeroni, lonselo lili m'manja mwa Akanani. Olamulira dziko la Afilisti akukhala ku Gaza, ku Asidodi, ku Asikeloni, ku Gati ndi ku Ekeroni), ndiponso dziko la Avimu chakumwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuchokera ku mtsinje wa Sihori kummawa kwa Igupto mpaka kumpoto kwa dziko la Ekroni. Madera onse amawerengedwa kuti ndi a Akanaani ngakhale amalamulidwa ndi mafumu asanu a Afilisti a ku Gaza, Asidodi, Asikeloni, Gati, Ekroni ndi Agiti, komanso ku Avimu ku chigawo cha kumpoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuyambira Sihoro wokhala cakuno ca Aigupto mpaka malire a Ekironu kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asekelo, a ku Giti, ndi a ku Ekiro, ndi Ahivi;