Joshua 13:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lidaphatikizaponso theka la Giliyadi, pamodzi ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda yaikulu ya mfumu Ogi wa ku Basani. Mizinda imeneyi idapatsidwa kwa mabanja a Makiri mwana wa Manase, kuti ikhale choloŵa cha hafu la Amakiri malinga ndi mabanja ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, midzi ya ufumu wa Ogi m'Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Derali linaphatikizanso theka la Giliyadi pamodzi ndi Asiteroti ndi Ederi, mizinda yayikulu ya mfumu Ogi wa Basani. Mizinda imeneyi inapatsidwa kwa mabanja a Makiri, mwana wa Manase kuti ikhale cholowa cha theka la ana a Makiri, malinga ndi mabanja awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi Gileadi logawika pakati, ndi Asitarotu ndi Edrei, midzi ya ufumu wa Ogi m'Basana, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.