Joshua 13:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komatu Mose sadaŵapatse dziko a fuko la Levi. Mose adaŵauza Aleviwo kuti choloŵa chao ndi gawo la zopereka zimene anthu ankapereka ngati nsembe zopsereza kwa Chauta, monga momwe Chautayo adaauzira Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma fuko la Levi, Mose analibe kulipatsa cholowa: Yehova Mulungu wa Israele, ndiye cholowa chao, monga ananena nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu Mose sanapereke malo kwa fuko la Levi. Mose anawawuza kuti zopereka zimene anthu ankapereka kwa Yehova ndizo cholowa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pfuko la Levi, Mose analibe kulipatsa colowa: Yehova Mulungu wa lsrayeli, ndiye colowa cao, monga ananena nao.