Joshua 13:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palinso dziko la Asidoni, amene akukhala m'dera lamapiri, pakati pa phiri la Lebanoni ndi la Misirefoti-Maimu. Anthu onsewo Ine Mulungu ndidzaŵapirikitsa m'mene Aisraele azikafika. Uŵagaŵire Aisraele maiko ameneŵa kuti akhale choloŵa chao, potsata zomwe ndakulamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Palinso anthu okhala mʼchigawo cha ku mapiri kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Misirefoti-Maimu, Ine ndidzawapirikitsa pamene Aisraeli azidzalowa. Tsono uwagawire Aisraeli dziko limeneli kuti likhale cholowa chawo monga momwe ndakulamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebano, mpaka Misirepotumaimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israyeli, koma limeneli uwagawire Aisrayeli, likhale colowa cao, monga ndinakulamulira.