Joshua 13:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndiponso theka lina lija la fuko la Manase adalandira dziko lao cha kuvuma kwa Yordani. Dziko limeneli ndilo lija adaŵapatsa Mose mtumiki wa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi pamodzi ndi theka lina la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa. Cholowa chawocho chinali kummawa kwa mtsinje wa Yorodani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira colowa cao, cimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordano kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;