Joshua 13:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko laolo lidayambira ku Aroere, mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso ku mzinda wokhala pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikiza dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba kukafika ku Diboni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mudzi uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lawolo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikizanso dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba mpaka ku Diboni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuyambira pa Aroeri, wokhala m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi mudzi uti pakati pa cigwa, ndi cidikha conse ca Medeba mpaka ku Diboni;