Joshua 14:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maiko amene Aisraele adalandira ku Kanani adagaŵidwa motere: Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mabanja a mafuko a Aisraele, onseŵa ndiwo adagaŵa maikowo, kugaŵira Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo awa ndi maiko ana a Israele anawalanda m'dziko la Kanani, amene Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, anawagawira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Umu ndi mmene Aisraeli analandirira cholowa chawo mʼdziko la Kanaani. Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni pamodzi ndi akuluakulu a mafuko a Israeli ndiwo anagawa dzikolo kugawira Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo awa ndi maiko ana a Israyeli anawalanda m'dziko la Kanani, amene Eleazare wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli, anawagawira.