Joshua 14:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kalebe adapitiriranso kunena kuti, “Koma tsopano, papita zaka 45 Chauta atauza kale Mose zimenezi. Taonani, ndili ndi zaka 85 tsopano,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, taonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi makumi anai ndi zisanu kuyambira nthawi ija Yehova ananena kwa Mose mau awa, poyenda Israele m'chipululu; ndipo tsopano taonani, ndine wa zaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono papita zaka 45 chiyankhulire Yehova zimenezi kwa Mose. Nthawi imeneyo nʼkuti Aisraeli akuyendayenda mʼchipululu. Yehova wandisunga ndipo tsopano ndili ndi zaka 85.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, taonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi mak umi anai ndi zisanu kuyambira nthawi ija Yehova ananena kwa Mose mau awa, poyenda Israyeli m'cipululu; ndipo tsopano taonani, ndine wa zaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lero lino.