Joshua 14:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
komabe ndikadali ndi mphamvu lero, monga ndidaaliri muja, pamene Mose adandituma. Ndikadali wamphamvu, mwakuti ndingathe kumenya nkhondo ndithu, ndiponso ndingathe kuchita zina zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma lero lino ndili wamphamvu monga tsiku lija anandituma Mose; monga mphamvu yanga pamene paja, momwemo mphamvu yanga tsopano, kugwira nkhondo, ndi kutuluka ndi kulowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe ndikanali ndi mphamvu lero, monga ndinalili tsiku lija Mose anandituma. Ndili ndi mphamvu moti ndikhoza kupita ku nkhondo kapena kuchita kanthu kena kalikonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma lero lino ndiri wamphamvu monga tsiku lija anandituma Mose; monga mphamvu yanga pamene paja, momwemo mphamvu yanga tsopano, kugwira nkhondo, ndi kuturuka ndi kulowa.