Joshua 14:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano mundigaŵire dziko lamapiri lomwe Chauta adandilonjezeratu. Paja mudamva kuti Aanaki, anthu amphamvu, adalipodi kumeneko m'mizinda yao yamalinga. Komabe mwina Chauta adzakhala nane, ndipo ndidzaŵapirikitsa monga momwe Chauta adanenera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi midzi yaikulu ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ndipatseni dziko la ku mapiri limene Yehova anandilonjeza tsiku lija. Inu munamva nthawi ija kuti Aanaki anali kumeneko ndipo kuti mizinda yawo inali ikuluikulu ndi yotetezedwa. Komabe Yehova atakhala nane ndidzawathamangitsa monga Iye ananenera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi midzi yaikuru ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova.