Joshua 14:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zisanachitike zimenezi, Hebroni ankatchedwa Kiriyati-Ariba. Arabayo ndiye anali wotchuka kopambana pakati pa Aanaki. Pambuyo pake m'dziko lonselo mudakhala mtendere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kale dzina la Hebroni linali mudzi wa Araba, ndiye munthu wamkulu pakati pa Aanaki. Ndipo dziko linapumula nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Hebroni ankatchedwa Kiriati Ariba chifukwa cha Ariba amene anali munthu wamphamvu kwambiri pakati pa Aanaki). Ndipo kenaka mʼdziko monse munakhala mtendere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kale dzina la Hebroni linali mudzi wa Ariba, ndiye munthu wamkuru pakati pa Aanaki. Ndipo dziko linapumula nkhondo.