Joshua 14:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono fuko la Yosefe adaligaŵa paŵiri, Manase ndi Efuremu. Alevi sadalandire gawo lililonse la dziko. Adangolandira mizinda kuti azikhalamo ndi timaiko todyetsamo zoŵeta zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ana a Yosefe ndiwo mafuko awiri, Manase ndi Efuremu; ndipo sanawagawire Alevi kanthu m'dziko, koma midzi yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi chuma chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono fuko la Yosefe analigawa pawiri, Manase ndi Efereimu. Mose sanawagawire malo mabanja a fuko la Levi, koma iwo anangolandira mizinda imene ankakhalamo pamodzi ndi malo amene ankawetako nkhosa ndi ngʼombe zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ana a Yosefe ndiwo mapfuko awiri, Manase ndi Efraimu; ndipo sanawagawira Alevi kanthu m'dziko, koma midzi yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi cuma cao.