Joshua 14:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a fuko la Yuda adabwera kwa Yoswa ku Giligala. Kalebe mmodzi mwa iwowo, mwana wa Yefune Mkenizi, adauza Yoswa kuti, “Inu mukudziŵa zimene Chauta adauza Mose, munthu wa Mulungu uja, za inu ndi ine ku Kadesi-Baranea.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa chimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu m'Kadesi-Baranea.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anthu a fuko la Yuda anabwera kwa Yoswa ku Giligala, ndipo Kalebe mwana wa Yefune Mkeni anati kwa iye, “Inu mukudziwa zimene Yehova ananena kwa Mose munthu wa Mulungu za inu ndi ine ku Kadesi Barinea.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa cimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu m'KadesiBarinea.