Joshua 14:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imene ija ndinali ndi zaka makumi anai pamene Mose mtumiki wa Chauta adandituma kuchokera ku Kadesi-Baranea kukazonda dziko lija. Nditabwerako, ndidamuuzadi zoona zonse zimene ndidaona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinali ine wa zaka makumi anai muja Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi-Baranea, kukazonda dziko; ndipo ndinambwezera mau, monga momwe anakhala mumtima mwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imene Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi Barinea kudzayendera dzikoli ndinali ndi zaka makumi anayi. Ndipo nditabwerako ndinamuwuza zoona zokhazokha monga momwe ndinaonera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinali ine wa zaka makumi anai muja Mose mtumiki wa Yehova anandituma kucokera ku Kadesi-Barinea, kukazonda dziko; ndipo ndinambwezera mau, monga momwe anakhala mumtima mwanga.