Joshua 15:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kumene adazungulira cha kuzambwe kwa Baala, kuloza ku dziko lamapiri la Seiri. Adapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu, (ndiye kuti Kesaloni), natsikira ku Betesemesi mpaka kubzola Timna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kunka kumadzulo, kuphiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Betesemesi, napitirira ku Timna;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera kumeneko anazungulira cha kumadzulo ku Baalahi mpaka ku phiri la Seiri. Anapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu (lomwe ndi Kesaloni). Anapitirirabe kutsika ku Beti Semesi ndi kuwolokera ku Timna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kumka kumadzulo, ku phiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Beti-semesi, napitirira ku Timina;