Joshua 15:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe Chauta adalamulira Yoswa, gawo lina la dziko la fuko la Yuda lidapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune. Yoswa adampatsa Kiriyati-Ariba ndiye kuti Hebroni. (Araba anali bambo wa Anaki).
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Potsata lamulo la Yehova, Yoswa anapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune gawo lina la dziko la Yuda dera la Kiriati Ariba, limene ndi Hebroni. (Ariba anali gogo wa Aanaki).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.