Joshua 15:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbale wake wa Kalebe, Otiniyele, mwana wa Kenazi, adaulanda mzindawo. Choncho Kalebe adampatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Otiniyele mwana wa Kenazi, mbale wake wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wake akhale mkazi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Otanieli, mwana wa mʼbale wa Kalebe, Kenazi, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Otiniyeli mwana wa Kenazi, mbale wace wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wace akhale mkazi wace.