Joshua 15:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adayankha kuti, “Ndimati mundipatseko mphatso. Popeza kuti mwandikhazika m'dziko la Negebu lopanda madzi, mundipatsenso akasupe a madzi.” Choncho Kalebe adampatsa akasupe akumtunda ndi akuchigwa omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwela, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.