Joshua 15:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
napita cha kumwera kokhakokha kuyambira ku chikweza cha ku Akarabimu, nkudzera pa mpata wa mapiri a ku Zini. Kuchokera kumeneko, adabzola cha kumwera kwa Kadesi-Baranea, kupitirira Hezironi mpaka ku Adara, ndi kutembenukira ku Karaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
natuluka kumwera kwa chikweza cha Akarabimu, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Baranea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kudutsa cha kummwera ku Akirabimu, nʼkupitirira mpaka ku Zini. Kuchokera pamenepo nʼkumapita cha kummwera kwa Kadesi Barinea, kudutsa Hezironi mpaka ku Adari ndi kutembenuka mpaka ku Karika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
naturuka kumwela kwa cikweza ca Akarabi, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Barinea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;