Joshua 15:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalandiranso mizinda yaikulu ya Asidodi ndi Gaza, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Malire ake adafika ku mtsinje wa ku Ejipito, ndipo mpaka ku Nyanja Yaikulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Asidodi, midzi yake ndi milaga yake; Gaza, midzi yake ndi milaga yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panalinso mizinda ya Asidodi ndi Gaza pamodzi ndi midzi yawo. Malire ake anafika ku mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Asidodo, midzi yace ndi miraga yace; Gaza, midzi yace ndi miraga yace; mpaka mtsinje wa Aigupto, ndi nyanja yaikuru ndi malire ace.