Joshua 15:63 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu a fuko la Yuda sadathe kupirikitsa Ayebusi amene ankakhala ku Yerusalemu. Ndipo mpaka pano Ayebusiwo amakhalabe mu Yerusalemu, pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yuda sanathe kuthamangitsa Ayebusi amene amakhala ku Yerusalemu, ndipo mpaka lero Ayebusi akukhala komweko pamodzi ndi Ayudawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ana a Yuda sanakhoza kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.