Joshua 15:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo malirewo adachokeranso ku chigwa cha Mavuto mpaka ku Debiri, mpakanso kumpoto kuloŵera ku Giligala, kuyang'anana ndi chikweza cha Adumimupasi cha ku mbali yakumwera ya chigwa. Tsono adapitiriranso ku akasupe a Enisemesi, natulukira ku Enirogele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nakwera malire kunka ku Debiri, kuchokera ku chigwa cha Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa chikweza cha Adumimu, ndiko kumwera kwa mtsinje; napitirira malire kunka ku madzi a Enisemesi, ndi matulukiro ake anali ku Enirogele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo malirewo anachokeranso ku chigwa cha Akori mpaka ku Debri, kuchokera ku chigwa cha Akori ndi kutembenukira kumpoto ku Giligala, dera limene linayangʼanana ndi msewu wa Adumimu kummwera kwa chigwa. Anapitirira mpaka ku madzi a ku Eni Semesi ndi kutulukira ku Eni Rogeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nakwera malire kumka ku Dibiri, kucokera ku cigwa ca Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa cikweza ca Adumi, ndiko kumwela kwa mtsinje; napitirira malire kumka ku madzi a Enisemesi, ndi maturukiro ace anali ku Eni-rogeli;