Joshua 15:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adakwera kubzola chigwa cha mwana wa Hinomu cha mbali ya kumwera kwa Ayebusi, (ndiye kuti ku Yerusalemu). Malirewo adapitirira kukafika pamwamba pa phiri moyang'anana ndi chigwa cha Hinomu chakuzambwe, ku mathero akumpoto a chigwa cha Refaimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anapitirira mpaka ku chigwa cha Hinomu mbali ya kummwera kwa mzinda wa Ayebusi (mzinda wa Yerusalemu). Kuchokera kumeneko anakwera mpaka pamwamba pa phiri kumadzulo kwa chigwa cha Hinomu cha kumpoto kwenikweni kwa chigwa cha Refaimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nakwera malire kumka ku cigwa ca mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwela, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kumka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa cigwa ca Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ace a cigwa ca Refai kumpoto,