Joshua 15:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adachokeranso pamwamba pa phiri, nakafika mpaka ku akasupe a Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya ku phiri la Efuroni. Kuchoka uko nkutsikira ku Baala, (ndiye kuti Kariyati-Yearimu),
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba pa phiri mpaka chitsime cha madzi cha Nefitowa, natulukira malire kumidzi ya phiri la Efuroni; ndipo analemba malire kunka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anachokeranso pamwamba pa phiri, kukafika mpaka ku akasupe a ku Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya phiri la Efroni, ndi kutsikira ku Baalahi (ndiye Kiriati Yearimu).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba pa phiri mpaka citsime ca madzi ca Nefitoa, naturukira malire ku midzi ya phiri la Efroni; ndipo analemba malire kumka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.