Joshua 16:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komatu Akanani amene ankakhala ku Gezere, Aefuremu sadaŵapirikitse, kotero kuti Akanani ameneŵa alipobe pakati pa Aefuremu mpaka lero lino. Komabe Akananiwo ankakakamizidwa kugwira ntchito yathangata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sanaingitse Akanani akukhala m'Gezere; koma Akanani anakhala pakati pa Efuremu, kufikira lero lino, nawaumiriza kugwira ntchito yathangata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo sanapirikitse Akanaani amene amakhala ku Gezeri ndipo mpaka lero Akanaani akukhala pakati pa Aefereimu koma amagwira ntchito ngati akapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo a sanaingitsa Akanani akukhala m'Gezeri; koma Akanani anakhala pakati pa Efraimu, kufikira lero lino, nawasonkhera msonkho.