Joshua 16:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono lidapitirira ndithu kuzambwe, kudera la Ayafaleti, mpaka kufika kunsi kwa Betehoroni. Kuchokera kumeneko malire ake adalunjika ku Gezere, nakalekeza mpaka ku nyanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
natsikira kumadzulo kunka ku malire a Ayafileti, ku malire a Betehoroni wa kunsi, ndi ku Gezere; ndi matulukiro ake anali kunyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malirewo anatsikira cha kumadzulo kwa dziko la Yafuleti mpaka ku chigawo cha kumunsi kwa Beti-Horoni. Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Gezeri nʼkuthera ku Nyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
natsikira kumadzulo kumka ku malire a Ayafeleti, ku malire a Beti-horoni wa kunsi, ndi ku Gezeri; ndi maturukiro ace anali kunyanja.