Joshua 16:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malirewo adaloŵera kuzambwe kuchokera ku Tapuwa mpaka ku mtsinje wa Kana, ndi kutsikira mpaka ku nyanja. Dziko limenelo ndilo lidapatsidwa kwa mabanja a Aefuremu kuti likhale choloŵa chao,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuyambira ku Tapuwa malire anamuka kumadzulo ku mtsinje wa Kana; ndi matulukiro ake anali kunyanja. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Efuremu monga mwa mabanja ao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera ku Tapuwa anapita kumadzulo mpaka ku mtsinje wa Kana ndi kukathera ku nyanja. Dziko ili linali cholowa cha mabanja afuko la Efereimu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuyambira ku Tapua malire anamuka kumadzulo ku mtsinje wa Kana; ndi maturukiro ace anali kunyanja. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Efraimu monga mwa mabanja ao;