Joshua 17:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gawo lina la dzikolo lidapatsidwa kwa fuko la Manase amene anali mwana wachisamba wa Yosefe. Makiri, kholo la anthu okhala ku Giliyadi, ndiye anali mwana wachisamba wa Manase. Makiri analinso msilikali, motero maiko aŵa, Giliyadi ndi Basani, adapatsidwa kwa iyeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gawo lina la dzikolo linapatsidwa kwa mabanja ena a fuko la Manase, mwana woyamba kubadwa wa Yosefe. Makiri anali mwana woyamba kubadwa wa Manase ndiponso kholo la anthu okhala ku Giliyadi. Popeza kuti iye anali munthu wankhondo, analandira Giliyadi ndi Basani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Gawo la pfuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Gileadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Gileadi ndi Basana.