Joshua 17:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Efuremu anali kumwera, Manase anali kumpoto, ndipo Nyanja Yaikulu inali malire akuzambwe. Malirewo adakafika ku Asere kumpoto chakuzambwe ndi ku Isakara kumpoto chakuvuma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kumwera nkwa Efuremu ndi kumpoto nkwa Manase, ndi malire ake ndi nyanja; ndi kumpoto anakomana ndi Asere, ndi kum'mawa anakomana ndi Isakara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko la kummwera linali la Efereimu ndipo la kumpoto linali la Manase. Dziko la Manase linafika ku nyanja ndipo linachita malire ndi Aseri, kumpoto ndiponso Isakara, kummawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kumwera nkwa Efraimu ndi kumpoto nkwa Manase, ndi malire ace ndi nyanja; ndi kumpoto anakomana ndi Aseri, ndi kum'mawa anakomana ndi Isakara.