Joshua 17:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'dziko la Isakara ndi la Asere munalinso gawo lina la Manase lotchedwa Beteseani, kuphatikizapo midzi yozungulira. Panalinso Akanani amene ankakhala ku Ibleamu, ku Dori mzinda wa m'mbali mwa nyanja, ku Endori, ku Taana ndi ku Megido, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'Isakara ndi m'Asere Manase anali nao Beteseani ndi midzi yake, ndi Ibleamu ndi midzi yake, ndi nzika za Dori ndi midzi yake, ndi nzika za Endori ndi midzi yake, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yake, ndi nzika za Megido ndi midzi yake; dziko la mapiri atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼdziko la Isakara ndi Aseri, Manase analinso ndi mizinda ya Beti-Seani ndi Ibuleamu pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. Panalinso Akanaani amene ankakhala ku Dori, Endori, Taanaki ndi Megido pamodzi ndi mizinda yozungulira (wachitatu pa mʼndandandawu ndi Nafati Dori).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'Isakara ndi m'Aseri Manase anali nao Betiseani ndi midzi yace, ndi Ibleamu ndi midzi yace, ndi nzika za Doro ndi midzi yace, ndi nzika za Eni-doro ndi midzi yace, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yace, ndi nzika za Megido ndi midzi yace; dziko la mapiri atatu.