Joshua 17:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe anthu a fuko la Manase sadathe kuŵapirikitsa Akanani okhala m'mizinda imeneyo. Motero Akananiwo adangokhalabe komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ana a Manase sanathe kuingitsa a m'midzi aja, popeza Akanani anafuna kukhala m'dziko lija.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe anthu a fuko la Manase sanathe kuwapirikitsa anthu okhala mʼmizinda imeneyi. Choncho Akanaani anakhalabe mʼmizindayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ana a Manase sanatha kuingitsa a m'midzi aja, popeza Akananjanafuna kukhala m'dziko lija.