Joshua 17:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yoswa adaŵayankha kuti, “Ngati mulipo ambiri, ndipo ngati dziko lamapiri la Efuremulo likucheperani, loŵani ku nkhalango, mudule mitengo ndi kudzikonzera malo oti mukhalepo m'dziko la Aperizi ndi Arefaimu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m'dziko la Aperizi ndi la Arefaimu; akakucheperani malo kuphiri la Efuremu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswa anayankha kuti, “Ngati muli ambiri ndipo dziko la ku mapiri la Efereimu lakucheperani kwambiri, lowani ku nkhalango mudule mitengo, mudzikonzere malo akuti mukhalemo, mʼdziko la Aperezi ndi Arefai.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m'dziko la Aperizi ndi la Arefai; akakuceperani malo ku phiri la Efraimu.