Joshua 17:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo zidzukulu za Yosefezo zidati, “Zoonadi dziko lamapirilo silingatikwanire ife, komanso Akanani amene ali ku zigwa ali ndi magaleta achitsulo, ngakhale amene ali ku Beteseani ndi ponse pozungulira, ndiponso amene ali m'chigwa cha Yezireele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Yosefe anati, Ku phiriko sikudzatifikira; ndipo Akanani onse akukhala m'dziko la chigwa ali nao magaleta achitsulo, iwo akukhala m'Beteseani, ndi midzi yake ndi iwo omwe akukhala m'chigwa cha Yezireele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono zidzukulu za Yosefe zinati, “Dziko la ku mapiri ndi losatikwaniradi, komanso Akanaani onse amene akukhala ku chigwa pamodzi ndi amene akukhala ku Beti-Seani ndi madera awo ndiponso amene ali ku chigwa cha Yezireeli ali ndi magaleta azitsulo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Yosefe anati, Kuphiriko sikudzatifikira; ndipo Akananionse akukhala m'dziko la cigwa ali nao magareta acitsulo, iwo akukhala m'Bete-Seani, ndi midzi yace ndi iwo omwe akukhala m'cigwa ca Yezereli.