Joshua 17:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzalandiradi dziko lamapirilo. Ngakhale lili ndi nkhalango, inuyo mudzadula mitengo, ndipo mudzalandira dziko lonselo kuti likhale lanu. Akanani mudzaŵapirikitsa, ngakhale ali ndi magaleta achitsulo ndiponso ngakhale iwo ngamphamvu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma kuphiriko kudzakhala kwanu pakuti pangakhale mpa mitengo, mudzisweretu minda, ndi matulukiro ake adzakhala anu; pakuti mudzaingitsa Akanani angakhale ali nao magaleta achitsulo, angakhale ali amphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
dziko la ku mapiri lidzakhalanso lanu. Ngakhale kuti ndi nkhalango yokhayokha koma inu mudzadula mitengo yake ndipo lidzakhala lanu mpaka kumapeto. Ngakhale kuti Akanaani ali ndi magaleta azitsulo ndiponso kuti iwo ndi amphamvu, koma inu mudzawapirikitsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma kuphiriko kudzakhala kwanu pakuti pangakhale mpa mitengo, mudzisweretu minda, ndi maturukiro ace adzakhala anu; pakuti mudzaingitsa Akanani angakhale ali nao magareta acitsulo, angakhale ali amphamvu.